Esther 1:16 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi Memukana anati, pamaso pa mfumu ndi akalonga, Vasiti mkazi wamkulu sanalakwire mfumu yekha, komanso akalonga onse, ndi mitundu yonse ya anthu okhala m'maiko onse a mfumu Ahasuwero.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Memukani anayankha pa maso pa mfumu ndi olemekezeka anzake kuti, “Mfumukazi Vasiti sanalakwire mfumu yokha, koma walakwiranso olemekezeka onse ndi anthu onse okhala mʼzigawo zonse za mfumu Ahasiwero.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi Memukana anati pamaso pa mfumu ndi akalonga, Vasiti mkazi wamkuru sanalakwira mfumu yekha, komanso akalonga onse, ndi mitundu yonse ya anthu okhala m'maiko onse a mfumu Ahaswero.