Esther 1:19 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chikakomera mfumu, atuluke mau achifumu pakamwa pake, nalembedwe m'malamulo a Apersiya ndi Amediya, angasinthike, kuti Vasiti asalowenso pamaso pa mfumu Ahasuwero; ndi mfumu aninkhe chifumu chake kwa mnzake womposa iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Choncho, ngati chikukomerani mfumu, lamulirani kuti Vasiti asadzaonekerenso pamaso pa mfumu Ahasiwero. Lamuloli lilembedwe mʼmabuku a malamulo a Aperezi ndi Amedi kuti lisadzasinthike. Pamalo pa Vasiti ngati mfumukazi payikidwepo mkazi wina amene ali bwino kuposa iye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cikakomera mfumu, aturuke mau acifumu pakamwa pace, nalembedwe m'malamulo a Aperisiya ndi Amediya, angasinthike, kuti Vasiti asalowenso pamaso pa mfumu Ahaswero; ndi mfumu aninkhe cifumu cace kwa mnzace womposa iye.