Esther 1:3 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chaka chachitatu cha ufumu wake, anakonzera madyerero akalonga ake onse, ndi omtumikira; amphamvu a Persiya ndi Mediya, omveka ndi akalonga a maikowo anakhala pamaso pake,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo mʼchaka chachitatu cha ufumu wake anakonza phwando la olemekezeka ndi nduna zake. Atsogoleri a nkhondo a ku Peresiya ndi Mediya, anthu olemekezeka pamodzi ndi nduna za mʼzigawo zonse anasonkhana kwa iye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
caka cacitatu ca ufumu wace, anakonzera madyerero akalonga ace onse, ndi omtumikira; amphamvu a Perisiya ndi Mediya, omveka ndi akalonga a maikowo anakhala pamaso pace,