Esther 1:5 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atatha masikuwa, mfumu inakonzera madyerero anthu onse okhala m'chinyumba cha ku Susa, akulu ndi ang'ono, masiku asanu ndi awiri, ku bwalo la munda wa maluwa wa ku chinyumba cha mfumu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atatha masiku amenewa, kwa masiku ena asanu ndi awiri mfumu inakonzanso phwando la anthu onse okhala mu mzinda wa Susa kuyambira anthu olemekezeka mpaka anthu wamba ku bwalo la munda la nyumba yake yaufumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atatha masikuwa, mfumu inakonzera madyerero anthu onse okhala m'cinyumba ca ku Susani, akulu ndi ang'ono, masiku asanu ndi awiri, ku bwalo la munda wa maluwa wa ku cinyumba ca mfumu;