Esther 2:12 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kunafika tsono kulowa kwake kwa namwali aliyense, kuti alowe kwa mfumu Ahasuwero, atamchitira monga mwa lamulo la akazi, miyezi khumi ndi iwiri; pakuti ankakwaniritsa masiku a mayeretsedwe ao motero, miyezi isanu ndi umodzi ndi mafuta a mure, ndi miyezi isanu ndi umodzi ndi zonunkhira bwino, ndi zoyeretsa akazi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono nthawi inkafika kuti namwali aliyense akaonekere kwa mfumu Ahasiwero, pakutha pa miyezi khumi ndi iwiri yomwe inakhazikitsidwa kuti amayi azidzikongoletsa. Pa miyezi isanu ndi umodzi ankadzola mafuta a mure ndipo pa miyezi isanu ndi umodzi inayo ankadzola zonunkhira ndi zokongoletsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kunafika tsono kulowa kwace kwa namwali ali yense, kuti alowe kwa mfumu Ahaswero, atamcitira monga mwa lamulo la akazi, miyezi khumi ndi iwiri; pakuti adafokwaniritsa masiku a mayeretsedwe ao motero, miyezi isanu ndi umodzi ndi mafuta a mure, ndi miyezi isanu ndi umodzi ndi zonunkhira bwino, ndi zoyeretsa akazi.