Esther 2:14 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Madzulo ake analowamo, nabwera m'mawa mwake kunka kunyumba yachiwiri ya akazi, amsunge Saasigazi mdindo wa mfumu, wosunga akazi aang'ono a mfumu; iyeyu sanalowenso kwa mfumu, koma akakondwera naye mfumu, ndi kumuitana kumtchula dzina lake, ndiko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ankalowa madzulo kwa mfumu ndi kutuluka mmawa kupita ku nyumba ina yosungira akazi yomwe ankayangʼanira ndi Saasigazi, mdindo wofulidwa wa mfumu amene amayangʼanira akazi a mfumu. Namwali sankabwerera kwa mfumu pokhapokha amukomere mtima ndi kumuyitana potchula dzina lake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Madzulo ace analowamo, nabwera m'mawa mwace kumka ku nyumba yaciwiri ya akazi, amsunge Saasigazi mdindo wa mfumu, wosunga akazi ang'ono a mfumu; iyeyu sanakwanso kwa mfumu, koma akakondwera naye mfumu, ndi kumuitana kumchula dzina lace, ndiko.