Esther 2:15 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pofika tsono kulowa kwake kwa Estere mwana wa Abihaili, atate wamng'ono wa Mordekai, amene adadzitengera akhale mwana wake, kuti alowe kwa mfumu, sanafune kanthu koma zonena Hegai mdindo wa mfumu wosunga akazi ndizo. Ndipo Estere anayamikizidwa pamaso pa onse ompenya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono inafika nthawi kuti Estere, mwana wamkazi wa Abihaili amenenso analeredwa ndi Mordekai amalume ake, alowe kwa mfumu. Iye sanapemphe kanthu kalikonse, koma anatenga zokhazo zimene ananena Hegai mdindo wofulidwa wa mfumu woyangʼanira nyumba yosungiramo akazi. Ndipo aliyense amene anamuona Estere, anasangalatsidwa naye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pofika tsono kulowa kwace kwa Estere mwana wa Abihaili, atate wamng'ono wa Moredekai, amene adadzitengera akhale mwana wace, kuti alowe kwa mfumu, sanafuna kanthu koma zonena Hege mdindo wa mfumu wosunga akazi ndizo. Ndipo Estere anayamikizidwa pamaso pa onse ompenya.