Esther 2:17 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu inakonda Estere koposa akazi onse, nalandira iye kuyanja ndi chifundo pamaso pake, koposa anamwali onse; motero anaika korona wachifumu pamutu pake, namuyesa mkazi wamkulu m'malo mwa Vasiti.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo mfumu inamukonda Estere koposa wina aliyense wa akazi aja, kotero inamukonda ndi kumukomera mtima koposa wina aliyense wa anamwali aja. Choncho anamumveka chipewa chaufumu pa mutu pake nakhala mfumukazi mʼmalo mwa Vasiti.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu inakonda Estere koposa akazi onse, nalandira iye kuyanja ndi cifundo pamaso pace, koposa anamwali onse; motero anaika korona wacifumu pamutu pace, namuyesa mkazi wamkuru m'malo mwa Vasiti.