Esther 2:3 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi mfumu aike oyang'anira m'maiko onse a ufumu wake, kuti asonkhanitse anamwali onse okongola m'chinyumba cha ku Susa, m'nyumba ya akazi; awasunge Hegai mdindo wa mfumu wosungira akazi, nawapatse zowayeretsa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu isankhe oyangʼanira pa chigawo chilichonse cha ufumu wake kuti abwere nawo pamodzi anamwali onse okongola ku nyumba yosungira akazi ku Susa. Hegai, mdindo wofulidwa wa mfumu, amene amayangʼanira amayi, akhale wosamalira anamwaliwa ndipo aziwapatsa mafuta odzola.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi mfumu aike oyang'anira m'maiko onse a ufumu wace, kuti asonkhanitse anamwali onse okongola m'cinyumba ca ku Susani, m'nyumba ya akazi; awasunge Hege mdindo wa mfumu wosungira akazi, nawapatse zowayeretsa;