Esther 3:12 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anaitana alembi a mfumu mwezi woyamba, tsiku lake lakhumi ndi chitatu, nalembera monga mwa zonse Hamani analamulira akazembe ndi ziwanga zoyang'anira maiko ali onse, ndi akalonga a mitundu iliyonse ya anthu, maiko ali onse monga mwa chilembedwe chao, ndi mitundu iliyonse ya anthu monga mwa chinenedwe chao; anazilemba m'dzina la mfumu Ahasuwero, nazisindikiza ndi mphete ya mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Alembi analemba zonse zimene Hamani analamula mʼmakalata opita kwa akazembe a mfumu, abwanamkubwa a zigawo zonse ndi kwa oyangʼanira mtundu uliwonse wa anthu. Kalatazo zinali za mʼchiyankhulo cha mtundu uliwonse ndipo zinalembedwa mʼdzina la Mfumu Ahasiwero ndi kusindikizidwa ndi mphete yake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anaitana alembi a mfumu mwezi woyamba, tsiku lace lakhumi ndi citatu, nalembera monga mwa zonse Hamani analamulira akazembe ndi ziwanga zoyang'anira maiko ali onse, ndi akalonga a mitundu iri yonse ya anthu, maiko ali onse monga mwa cilembedwe cao, ndi mitundu iri yonse ya anthu monga mwa cinenedwe cao; anazilemba m'dzina la mfumu Ahaswero, nazisindikiza ndi mphete ya mfumu.