Esther 3:2 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anyamata onse a mfumu okhala m'chipata cha mfumu anamweramira, namgwadira Hamani; pakuti mfumu idalamulira chotero za iye. Koma Mordekai sanamweramire kapena kumgwadira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atumiki onse a mfumu amene anali pa chipata cha nyumba ya mfumu ankagwadira ndi kuweramira Hamani monga mwa lamulo la mfumu. Koma Mordekai sankamugwadira kapena kumuweramira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anyamata onse a mfumu okhala m'cipata ca mfumu anamweramira, namgwadira Hamani; pakuti mfumu idalamulira cotero za iye. Koma Moredekai sanamweramira kapena kumgwadira.