Esther 3:7 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwezi woyamba ndiwo mwezi wa Nisani, chaka chakhumi ndi chiwiri cha mfumu Ahasuwero, anaombeza Puri, ndiwo ula, pamaso pa Hamani tsiku ndi tsiku, mwezi ndi mwezi, mpaka mwezi wakhumi ndi chiwiri, ndiwo mwezi wa Adara.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwezi woyamba, umene ndi mwezi wa Nisani, chaka cha khumi ndi chiwiri cha ufumu wa Ahasiwero anachita maere, otchedwa Purimu pamaso pa Hamani kuti apeze tsiku ndi mwezi woyenera. Ndipo maere anagwera pa mwezi wa khumi ndi chiwiri ndiwo mwezi wa Adara.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwezi woyamba ndiwo mwezi wa Nisani, caka cakhumi ndi ciwiri ca mfumu Ahaswero, anaombeza Puri, ndiwo ula, pamaso pa Hamani tsiku ndi tsiku, mwezi ndi mwezi, mpaka mwezi wakhumi ndi ciwiri, ndiwo mwezi wa Adara.