Esther 3:8 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Hamani anati kwa mfumu Ahasuwero, Pali mtundu wina wa anthu obalalika ndi ogawanikana mwa mitundu ya anthu m'maiko onse a ufumu wanu, ndi malamulo ao asiyana nao a anthu onse, ndipo sasunga malamulo a mfumu; chifukwa chake mfumu siiyenera kuwaleka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Hamani anakawuza mfumu Ahasiwero kuti, “Pali mtundu wina wa anthu umene unabalalika ndipo wamwazikana pa mitundu ina mʼzigawo zonse za ufumu wanu umene miyambo yawo ndi yosiyana ndi ya anthu ena onse ndiponso amene safuna kumvera malamulo a mfumu, kotero si chinthu cha phindu kuti mfumu iwalekerere anthu otere.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Hamani anati kwa mfumu Ahaswero, Pali mtundu wina wa anthu obalalika ndi ogawanikana mwa mitundu ya anthu m'maiko onse a ufumu wanu, ndi malamulo ao asiyana nao a anthu onse, ndipo sasunga malamulo a mfumu; cifukwa cace mfumu siiyenera kuwaleka.