Esther 4:1 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma podziwa Mordekai zonse zidachitikazi, Mordekai anang'amba zovala zake, navala chiguduli ndi mapulusa, natuluka pakati pa mudzi, nafuula, nalira kulira kwakukulu ndi kowawa,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mordekai atamva zonse zimene zinachitika, anangʼamba zovala zake, navala chiguduli ndi kudzola phulusa, ndipo analowa mu mzinda, akulira mokweza ndi mowawidwa mtima.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma podziwa Moredekai zonse zidacitikazi, Moredekai anang'amba zobvala zace, nabvala ciguduli ndi mapulusa, naturuka pakati pa mudzi, napfuula, nalira kulira kwakukuru ndi kowawa,