Esther 4:11 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akapolo onse a mfumu ndi anthu a m'maiko a mfumu adziwa kuti aliyense, ngakhale wamwamuna kapena wamkazi, akalowa kwa mfumu kubwalo la m'katimo wosaitanidwa, lamulo la pa iye ndi limodzi, ndilo kuti amuphe, akapanda mfumu kumloza ndi ndodo yachifumu yagolide kuti akhale ndi moyo; koma ine sanandiitane ndilowe kwa mfumu masiku awa makumi atatu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Atumiki onse amfumu ndi anthu a zigawo za mfumu ankadziwa kuti mwamuna kapena mkazi aliyense akalowa ku bwalo lake la mʼkati mosayitanidwa ndi mfumu pali lamulo limodzi: lamuloli ndi lakuti aphedwe. Zimasintha pokhapokha ngati mfumu iloza munthuyo ndi ndodo yagolide kuti akhale ndi moyo. Koma papita masiku makumi atatu ndisanayitanidwe ndi mfumu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akapolo onse a mfumu ndi anthu a m'maiko a mfumu adziwa kuti ali yense, ngakhale wamwamuna kapena wamkazi, akalowa kwa mfumu ku bwalo la m'katimo wosaitanidwa, lamulo la pa iye ndi limodzi, ndilo kuti amuphe, akapanda mfumu kumloza ndi ndodo yacifumu yagolidi kuti akhale ndi moyo; koma ine sanaodiitana ndilowe kwa mfumu masiku awa makumi atatu.