Esther 4:3 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi m'maiko monse, paliponse anafikapo mau a mfumu ndi lamulo lake, panali maliro akulu mwa Ayuda, ndi kusala, ndi kulira misozi, ndi kubuma; nagona m'chiguduli ndi mapulusa ambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chigawo chilichonse kumene mawu a mfumu ndi lamulo lake zinafika, kunali maliro akulu pakati pa Ayuda. Iwo ankasala zakudya, kulira mofuwula ndi kumadandaula. Ambiri anavala ziguduli ndi kudzola phulusa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi m'maiko monse, pali ponse anafikapo mau a mfumu ndi lamulo lace, panali maliro akuru mwa Ayuda, ndi kusala, ndi kulira misozi, ndi kubuma; nagona m'ciguduli ndi mapulusa ambiri.