Esther 4:5 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Estere anaitana Hataki mdindo wina wa mfumu, amene idamuika amtumikire, namuuza amuke kwa Mordekai, kuti adziwe ichi nchiyani ndi chifukwa chake ninji.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Estere anayitana Hataki, mmodzi wa adindo a mfumu ofulidwa amene anayikidwa kuti azimutumikira kuti apite kwa Mordekai kuti akamve chimene chimamuvuta komanso chifukwa chochitira zimenezi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Estere anaitana Hataki mdindo wina wa mfumu, amene idamuika amtumikire, namuuza amuke kwa Moredekai, kuti adziwe ici nciani ndi cifukwa cace ninji.