Esther 4:8 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anampatsanso chitsanzo cha lamulo lolembedwa adalibukitsa m'Susa, kuwaononga, achionetse kwa Estere, ndi kumfotokozera, ndi kumlangiza alowe kwa mfumu, kumpembedza, ndi kupempherera anthu ake kwa iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mordekai anamupatsanso imodzi mwa makalata a ulamuliro wonena za chiwembuchi amene anawasindikiza ku Susa kukamuonetsa ndi kumufotokozera zonse Estere. Anamuwuzanso kuti akamudandaulire kuti akapite kwa mfumu kukapempha chifundo ndi kuyidandaulira chifukwa cha anthu a mtundu wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anampatsanso citsanzo ca lamulo lolembedwa adalibukitsa m'Susani, kuwaononga, acionetse kwa Estere, ndi kumfotokozera, ndi kumlangiza alowe kwa mfumu, kumpembedza, ndi kupempherera anthu ace kwa iye.