Esther 5:1 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali tsiku lachitatu, Estere anavala zovala zake zachifumu, nakaimirira m'bwalo la m'kati la nyumba ya mfumu, popenyana pa nyumba ya mfumu; ndi mfumu inakhala pa mpando wake wachifumu m'nyumba yachifumu, pandunji polowera m'nyumba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku lachitatu Estere anavala zovala zake zaufumu ndipo anayima mʼbwalo la mʼkati la nyumba yaufumu choyangʼana ku chipinda chachikulu cha mfumu. Mfumu inakhala pa mpando waufumu mʼchipinda chachikulu moyangʼana ku chipata cholowera mʼnyumba yaufumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali tsiku lacitatu, Estere anabvala zobvala zace zacifumu, nakaimirira m'bwalo la m'kati la nyumba ya mfumu, popenyana pa nyumba ya mfumu; ndi mfumu inakhala pa mpando wace wacifumu m'nyumba yacifumu, pandunji polowera m'nyumba.