Esther 5:12 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Hamani anatinso, Ndiponso Estere mkazi wamkulu sanalole mmodzi yense alowe pamodzi ndi mfumu ku madyerero adakonzawo, koma ine ndekha; nandiitana mawanso pamodzi ndi mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Hamani anawonjeza kuti, “Ndipotu si zokhazi. Ndine ndekha amene ndayitanidwa pamodzi ndi mfumu kuphwando limene mfumukazi Estere anatikonzera. Ndipo mawa wandiyitananso pamodzi ndi mfumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Hamani anatinso, Ndiponso Estere mkazi wamkuru sanalola mmodzi yense alowe pamodzi ndi mfumu ku madyerero adakonzawo, koma ine ndekha; nandiitana mawanso pamodzi ndi mfumu.