Esther 5:14 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Zeresi mkazi wake, ndi mabwenzi ake onse ananena naye, Apange mtengo, msinkhu wake mikono makumi asanu, ndi mawa mukanene nayo mfumu kuti ampachike Mordekai pamenepo; nimulowe pamodzi ndi mfumu kumadyerero wokondwera. Ndipo ichi chidakomera Hamani, napangitsa anthu mtengowo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mkazi wake Zeresi ndi abwenzi ake onse aja anamuwuza kuti, “Anthu apange mtanda wotalika mamita 23 ndipo mmawa upemphe mfumu kuti anthu akhomerepo Mordekai. Kenaka upite ndi mfumu kuphwando mokondwa.” Hamani anakondwera ndi uphungu umenewu ndipo mtanda unapangidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Zeresi mkazi wace, ndi mabwenzi ace onse ananena naye, Apange mtengo, msinkhu wace mikono makumi asanu, ndi mawa mukanene nayo mfumu kuti ampacike Moredekai pamenepo; nimulowe pamodzi ndi mfumu kumadyerero wokondwera. Ndipo ici cidakomera Hamani, napangitsa anthu mtengowo.