Esther 5:2 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, pamene mfumu inaona Estere mkazi wamkuluyo alikuima m'bwalo, inamkomera mtima; ndi mfumu inamloza Estere ndi ndodo yachifumu yagolide inali m'dzanja lake. Nayandikira Estere, nakhudza nsonga ya ndodoyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu itaona Estere atayima mʼbwalomo inakondwera naye ndipo anamuloza ndi ndodo yagolide imene inali mʼdzanja lake. Choncho Estere anayandikira ndi kukhudza msonga ya ndodoyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, pamene mfumu inaona Estere mkazi wamkuruyo alikuima m'bwalo, inamkomera mtima; ndi mfumu inamloza Estere ndi ndodo yacifumu yagolidi inali m'dzanja lace. Nayandikira Estere, nakhudza nsonga ya ndodoyo.