Esther 5:3 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ninena naye mfumu, Mufunanji, Estere mkazi wamkulu? Pempho lanu nchiyani? Lidzaperekedwa kwa inu, kufikira limodzi la magawo awiri a ufumuwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka mfumu inati kwa iye, “Kodi mukufuna chiyani, inu mfumukazi Estere? Nanga pempho lanu ndi chiyani? Ngakhale mutapempha theka la ufumu, ndidzakupatsani.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ninena naye mfumu, Mufunanji, Estere mkazi wamkuru? pempho lanu nciani? lidzaperekedwa kwa inu, kufikira limodzi la magawo awiri a ufumuwo.