Esther 5:6 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu inati kwa Estere pa madyerero a vinyo, Pempho lanu nchiyani? Lidzaperekedwa kwa inu; mufunanji? Chidzachitika, kufikira limodzi la magawo awiri a ufumuwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akumwa vinyo, mfumu inamufunsano Estere kuti, “Kodi ukupempha chiyani tsopano? Chimene uti upemphe ndikupatsa. Chopempha chako ndi chiti? Ngakhale utafuna mpaka theka la ufumu, ndidzakupatsa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu inati kwa Estere pa madyerero a vinyo, Pempho lanu nciani? lidzaperekedwa kwa inu; mufunanji? cidzacitika, kufikira limodzi la magawo awiri a ufumuwo.