Esther 5:8 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ngati mfumu indikomera mtima, ngatinso chakomera mfumu kupereka pempho langa ndi kuchita chofuna ine, adze mfumu ndi Hamani ku madyerero ndidzawakonzera; ndipo mawa ndidzachita monga yanena mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati mwandikomera mtima mfumu ndiponso ngati chingakukondweretseni mfumu kundipatsa chimene ndapempha ndi kuchita zimene ndifuna, mubwere mawa inu mfumu ndi Hamani ku phwando limene ndidzakukonzerani. Ndipo ndidzakuyankhani mfumu funso lanu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ngati mfumu indikomera mtima, ngatinso cakomera mfumu kupereka pempho langa ndi kucita cofuna ine, adze mfumu ndi Hamani ku madyerero ndidzawakonzera; ndipo mawa ndidzacita monga yanena mfumu.