Esther 6:12 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mordekai anabweranso kuchipata cha mfumu. Koma Hamani anafulumira kunka kwao, wachisoni ndi wofunda mutu wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pambuyo pake Mordekai anabwerera ku chipata cha mfumu. Koma Hamani anapita msanga ku nyumba kwake, akulira, atafundira mutu wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Moredekai anabweranso ku cipata ca mfumu. Koma Hamani anafulumira kumka kwao, wacisoni ndi wopfunda mutu wace.