Esther 6:13 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Hamani anafotokozera Zeresi mkazi wake, ndi mabwenzi ake onse, zonse zidamgwera. Nanena naye anzeru ake, ndi Zeresi mkazi wake, Mordekai amene wayamba kutsika pamaso pake, akakhala wa mbumba ya Ayuda, sudzamlaka; koma udzagwada pamaso pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Hamani anawuza Zeresi mkazi wake ndi abwenzi ake onse zonse zinamuchitikira. Anthu ake anzeru ndi mkazi wake Zeresi anamuwuza kuti, “Popeza kuti Mordekai ndi Myuda amene mwayamba kale kugonja pamaso pake, ndiye kuti palibe chimene mungachitepo. Mudzagwa ndithu pamaso pake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Hamani anafotokozera Zeresi mkazi wace, ndi mabwenzi ace onse, zonse zidamgwera, Nanena naye anzeru ace, ndi Zeresi mkazi wace, Moredekai amene wayamba kutsika pamaso pace, akakhala wa mbumba ya Ayuda, sudzamlaka; koma udzagwada pamaso pace.