Esther 6:9 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
napereke chovala ndi kavalo m'dzanja la wina womveketsa wa akalonga a mfumu, naveke nacho munthu amene mfumu ikondwera kumchitira ulemu, namuyendetse pa kavaloyo m'khwalala la m'mudzi, nafuule pamaso pake, Azitero naye munthu amene mfumu ikondwera kumchitira ulemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo mupereke chovala cha ufumucho ndi kavalo kwa mmodzi wa akalonga a mfumu a ulemu kwambiri. Ameneyu amuveke chovalacho munthu amene mfumu yakondweretsedwa naye. Akavekedwa chovalachi amuyendetse mʼmisewu yonse ya mzinda atakwera pa kavalo wa mfumu. Kalongayu azifuwula patsogolo pa munthuyu kuti ‘Ichi ndi chimene mfumu yachita kwa munthu amene yafuna kumuchitira ulemu!’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
napereke cobvala ndi kavalo m'dzanja la wina womveketsa wa akalonga a mfumu, nabveke naco munthu amene mfumu ikondwera kumcitira ulemu, namuyendetse pa kavaloyo m'khwalala la m'mudzi, napfuule pamaso pace, Azitero naye munthu amene mfumu ikondwera kumcitira ulemu.