Esther 7:8 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nibwera mfumu kumunda wa maluwa wa kuchinyumba kulowanso m'nyumba munali madyerero a vinyo, napeza Hamani atagwa pa kama wokhalapo Estere. Niti mfumu, Kodi aumiriza mkazi wamkulu pamaso panga m'nyumba? Potuluka mau pakamwa pa mfumu anamphimba Hamani nkhope.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu itabwerera kuchokera ku munda wa maluwa wa nyumba yaufumu uja ndi kulowanso mʼchipinda chaphwando, anapeza Hamani atagona chafufumimba pa mpando wa khutagone pomwe Estere anakhalapo. Mfumu inayankhula mokweza kuti, “Kodi afunanso kuvula mfumukazi momukakamiza pamene ine ndili mʼnyumba?” Mfumu isanatsirize kuyankhula mawu awa, atumiki ake anaphimba nkhope ya Hamani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nibwera mfumu ku munda wa maluwa wa kucinyumba kulowanso m'nyumba munali madyerero a vinyo, napeza Hamani atagwa pa kama wokhalapo Estere. Niti mfumu, Kodi aumiriza mkazi wamkuru pamaso panga m'nyumba? Poturuka mau pakamwa pa mfumu anamphimba Hamani nkhope.