Esther 7:9 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati Haribona wina wa adindo okhala pamaso pa mfumu, Taonaninso, mtengowo msinkhu wake mikono makumi asanu, umene Hamani anaupangira Mordekai wonenera mfumu zokoma, uimiritsidwa m'nyumba ya Hamani. Niti mfumu, Mpachike pomwepo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Haribona, mmodzi wa adindo ofulidwa amene ankatumikira mfumu anati, “Mtanda wotalika mamita 23 uli mʼnyumba ya Hamani. Mtandawu, Hamani anapangira Mordekai, uja amene anapulumutsa mfumu ku chiwembu.” Mfumu inati, “Mpachikeni pamenepo!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati Haribona wina wa adindo okhala pamaso pa mfumu, Taonaninso, mtengowo msinkhu wace mikono makumi asanu, umene Hamani anaupangira Moredekai wonenera mfumu zokoma, uimiritsidwa m'nyumba ya Hamani. Niti mfumu, Mpacike pomwepo.