Esther 8:11 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
m'menemo mfumu inalola Ayuda okhala m'midzi iliyonse asonkhane, ndi kulimbikira moyo wao, kuononga, kupha, ndi kupulula mphamvu yonse ya anthu ndi ya dziko yofuna kuwathira nkhondo, iwo, ana ang'ono ao, ndi akazi ao, ndi kulanda zofunkha zao,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼmakalata amenewa mfumu inalola kuti Ayuda okhala mu mzinda uliwonse akhale ndi ufulu wokumana ndi kudzitchinjiriza komanso kuwononga, kupha ndi kufafaniziratu gulu lililonse la nkhondo la anthu a mtundu uliwonse kapena chigawo chimene chingawathire nkhondo. Ayudawo analoledwa kuwononga gulu lankhondo lija, ana awo ndi akazi awo komanso kuti afunkhe katundu wawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
m'menemo mfumu inalola Ayuda okhala m'midzi iri yonse asonkhane, ndi kulimbikira moyo wao, kuononga, kupha, ndi kupulula mphamvu yonse ya anthu ndi ya dziko yofuna kuwathira nkhondo, iwo, ana ang'ono ao, ndi akazi ao, ndi kulanda zofunkha zao,