Esther 8:13 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chitsanzo chake, cha lemboli, chakuti abukitse lamulo m'maiko onse, chinalalikidwa kwa mitundu yonse ya anthu, kuti, Ayuda akonzekeretu tsiku lijalo, kubwezera chilango adani ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mawu a mʼmakalatawo anayenera kudziwitsidwa kwa anthu a mtundu uliwonse mu chigawo chilichonse kuti ndi lamulo ndithu kwa anthu a mtundu uliwonse ndi kuti Ayuda adzakhale okonzeka pa tsikulo kulipsira kwa adani awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Citsanzo cace, ca lemboli, cakuti abukitse lamulo m'maiko onse, cinalalikidwa kwa mitundu yonse ya anthu, kuti, Ayuda akonzekeretu tsiku lijalo, kubwezera cilango adani ao.