Esther 8:15 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mordekai anatuluka pamaso pa mfumu wovala chovala chachifumu chamadzi ndi choyera, ndi korona wamkulu wagolide, ndi malaya abafuta ndi ofiirira; ndi mudzi wa Susa unafuula ndi kukondwera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mordekai anachoka pamaso pa mfumu atavala zovala zaufumu zooneka ngati mtambo ndi zofewa zoyera, chipewa chachikulu cha golide ndi mkanjo wapepo. Ndipo mzinda wa Susa unafuwula mokondwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Moredekai anaturuka pamaso pa mfumu wobvala cobvala cacifumu camadzi ndi coyera, ndi korona wamkuru wagolidi, ndi maraya abafuta ndi ofiirira; ndi mudzi wa Susani unapfuula ndi kukondwera.