Esther 8:17 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi m'maiko monse, ndi m'midzi yonse, mudafika mau a mfumu ndi lamulo lake, Ayuda anali nako kukondwera ndi chimwemwe, madyerero ndi tsiku lokoma. Ndipo ambiri a mitundu ya anthu a m'dziko anasanduka Ayuda; pakuti kuopsa kwa Ayuda kudawagwera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼchigawo chilichonse ndi mu mzinda uliwonse, kumene mawu a mfumu onena za lamulo lake anafika, kunali chimwemwe ndi chikondwerero pakati pa Ayuda. Linali tsiku la phwando ndi chikondwerero. Ndipo anthu ambiri a mitundu ina anazitcha Ayuda chifukwa anachita mantha ndi Ayudawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi m'maiko monse, ndi m'midzi yonse, mudafika mau a mfumu ndi lamulo lace, Ayuda anali nako kukondwera ndi cimwemwe, madyerero ndi tsiku lokoma. Ndipo ambiri a mitundu ya anthu a m'dziko anasanduka Ayuda; pakuti kuopsa kwa Ayuda kudawagwera.