Esther 8:3 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nanenanso Estere pamaso pa mfumu, nagwa ku mapazi ake, nalira misozi, nampembedza kuti achotse choipacho cha Hamani wa ku Agagi, ndi chiwembu adachipangira Ayuda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Estere anayankhulanso ndi mfumu ndipo anadzigwetsa pa mapazi ake. Uku akulira iye anapempha mfumu kuti iletse choyipa, makamaka chiwembu chimene Hamani Mwagagi anakonza kuti awononge a Yuda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nanenanso Estere pamaso pa mfumu, nagwa ku mapazi ace, nalira misozi, nampembedza kuti acotse coipaco ca Hamani wa ku Agagi, ndi ciwembu adacipangira Ayuda,