Esther 8:5 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati, Chikakomera mfumu, ndipo ngati yandikomera mtima, nichiyenera kwa mfumu, ngatinso ndimchititsa kaso, alembere chosintha mau a akalata a chiwembu cha Hamani mwana wa Hamedata wa ku Agagi, amene adawalembera kuononga Ayuda okhala m'maiko onse a mfumu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anati, “Ngati chikomera mfumu ndi kukukondweretsani, ngati pempho langa muliona kuti ndi loyenera ndi kuti mukondwera nane tsono mfumu ilole kuti lamulo lilembedwe kusintha mawu a mʼmakalata amene Hamani mwana wa Hamedata, Mwagagi, anatumiza ku zigawo zonse za mfumu. Paja Hamani analemba kuti Ayuda onse awonongedwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati, Cikakomera mfumu, ndipo ngati yandikomera mtima, niciyenera kwa mfumu, ngatinso ndimcititsa kaso, alembere cosintha mau a akalata a ciwembu ca Hamani mwana wa Hamedata wa ku Agagi, amene adawalembera kuononga Ayuda okhala m'maiko onse a mfumu;