Esther 8:9 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anaitana alembi a mfumu nthawi yomweyo, mwezi wachitatu, ndiwo mwezi wa Sivani, tsiku lake la makumi awiri ndi chitatu, monga mwa zonse Mordekai analamulira; nalembera kwa Ayuda, ndi kwa akazembe, ndi ziwanga, ndi akalonga a kumaiko, oyambira ku Indiya, ofikira ku Kusi, maiko zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi awiri, ku dziko lililonse monga mwa chilembedwe chao, ndi mtundu uliwonse monga mwa chinenedwe chao, ndi kwa Ayuda monga mwa chinenedwe chao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi yomweyo, pa tsiku la 23 la mwezi wachitatu wa Sivani, mfumu inayitana alembi ake. Analemba zonse zokhudza Ayuda monga ananenera Mordekai. Analembera akazembe, abwanamkubwa ndi nduna za zigawo 127 kuyambira ku India mpaka ku Kusi. Zimene analamula Mordekai zinalembedwa mʼzilembo za chigawo chilichonse ndi chiyankhulo cha mtundu uliwonse wa anthu. Ayudanso anawalembera mʼmalemba awo ndi chiyankhulo chawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anaitana alembi a mfumu nthawi yomweyo, mwezi wacitatu, ndiwo mwezi wa Sivani, tsiku lace la makumi awiri ndi citatu, monga mwa zonse Moredekai analamulira; nalembera kwa Ayuda ndi kwa akazembe, ndi ziwanga, ndi akalonga a kumaiko, oyambira ku Indiya, ofikira ku Kusi, maiko zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi awiri, ku dziko liri lonse monga mwa cilembedwe cao, ndi mtundu uli wonse monga mwa cinenedwe cao, ndi kwa Ayuda monga mwa cilembedwe cao, ndi monga mwa cinenedwe cao.