Esther 9:1 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwezi wakhumi ndi chiwiri tsono, ndiwo mwezi wa Adara, tsiku lake lakhumi ndi chitatu, mau a mfumu ndi lamulo lake ali pafupi kuchitika, tsikuli adani a Ayuda anayesa kuwachitira ufumu, koma chinasinthika; popeza Ayuda anachitira ufumu iwo odana nao;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa mwezi wa 12, mwezi wa Adara pa tsiku la 13 la mwezi womwewo, tsiku limene lamulo loyamba lija la mfumu linayembekezereka kuti litsatidwe, pamene adani a Ayuda anati awononge Ayudawo, zinthu zinasintha. Ayuda ndiwo anawononga adani awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwezi wakhumi ndi ciwiri tsono, ndiwo mwezi wa Adara, tsiku lace lakhumi ndi citatu, mau a mfumu ndi lamulo lace ali pafupi kucitika, tsikuli adani a Ayuda anayesa kuwacitira ufumu, koma cinasinthika; popeza Ayuda anacitira ufumu iwo odana nao;