Esther 9:12 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu inati kwa mkazi wamkulu Estere, Ayuda adapha, naononga amuna mazana asanu m'chinyumba cha ku Susa, ndi ana amuna khumi a Hamani; nanga m'maiko ena a mfumu munachitikanji? Pempho lanu ndi chiyani tsono? Lidzachitikira inu; kapena mufunanjinso? Kudzachitika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu inati kwa mfumukazi Estere, “Ayuda apha ndi kuwononga anthu 500 ndi ana khumi a Hamani mu likulu la mzinda wa Susa. Nanga ku zigawo zina zonse za mfumu achitako chiyani? Kodi tsopano ukupemphanso chiyani? Chimene ukupempha ndidzakupatsa. Kodi ukufuna chiyani? Chimene ukufuna ndidzakupatsa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu inati kwa mkazi wamkuru Estere, Ayuda adapha, naononga amuna mazana asanu m'cinyumba ca ku Susani, ndi ana amuna khumi a Hamani; nanga m'maiko ena a mfumu munacitikanji? pempho lanu ndi ciani tsono? lidzacitikira inu; kapena mufunanjinso? kudzacitika.