Esther 9:19 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake Ayuda a kumilaga, okhala m'midzi yopanda malinga, amaliyesa tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi wa Adara tsiku la kukondwera ndi madyerero, ndi tsiku lokoma, ndi lakutumizirana magawo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ichi ndi chifukwa chake Ayuda a ku midzi, amene amakhala mʼzithando amasunga tsiku la 14 la mwezi wa Adara ngati la madyerero ndi chikondwerero, tsiku lopatsana mphatso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace Ayuda a kumiraga, okhala m'midzi yopanda malinga, amaliyesa tsiku lakhumi ndi cinai la mwezi wa Adara tsiku la kukondwera ndi madyerero, ndi tsiku lokoma, ndi lakutumizirana magawo.