Esther 9:2 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pakuti Ayuda anasonkhana pamodzi m'midzi mwao, m'maiko onse a mfumu Ahasuwero, kuwathira manja ofuna kuwachitira choipa, ndipo palibe munthu analimbika pamaso pao; popeza kuopsa kwao kudawagwera mitundu yonse ya anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ayuda anasonkhana mʼmizinda ya zigawo zonse za Mfumu Ahasiwero kuthira nkhondo onse amene anafuna kuwawononga. Palibe amene akanalimbana nawo chifukwa anthu onse a mitundu ina anachita nawo mantha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pakuti Ayuda anasonkhana pamodzi m'midzi mwao, m'maiko onse a mfumu Ahaswero, kuwathira manja ofuna kuwacitira coipa, ndipo palibe munthu analimbika pamaso pao; popeza kuopsa kwao kudawagwera mitundu yonse ya anthu.