Esther 9:28 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi kuti masikuwa adzakumbukika ndi kusungika mwa mibadwo yonse, banja lililonse, dziko lililonse, ndi mudzi uliwonse; ndi kuti masiku awa sadzalekeka mwa Ayuda, kapena kusiyidwa chikumbukiro chao mwa mbeu yao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Azisunga ndi kukumbukira masiku amenewa mu mʼbado uliwonse ndi banja lililonse, mʼchigawo chilichonse ndi mu mzinda uliwonse. Ndipo Ayuda asadzasiye kukondwerera masiku a Purimuwa ndiponso zidzukulu zawo zisadzaleke kuwakumbukira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi kuti masikuwa adzakumbukika ndi kusungika mwa mibadwo yonse, banja liri lonse, dziko liri lonse, ndi mudzi uli wonse; ndi kuti masiku awa sadzalekeka mwa Ayuda, kapena kusiyidwa cikumbukilo cao mwa mbeu yao.