Exodus 1:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adaika akapitao ao oŵagwiritsa mwankhanza ntchito yolimba Aisraelewo, kuti pakutero aŵafooketse. Aisraele adamangira Faraoyo mizinda ya Pitomu ndi Ramsesi, kumene Aejipito ankasunga chakudya chao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Potero anawaikira akulu a misonkho kuti awasautse ndi akatundu ao. Ndipo anammangira Farao midzi yosungiramo chuma, ndiyo Pitomu ndi Ramsesi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero anayika akapitawo kuti aziwazunza ndi kuwagwiritsa ntchito yolemetsa mokakamiza. Iwo anamangira Farao mizinda ya Pitomu ndi Ramesesi kumene ankasungirako chakudya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Potero anawaikira akuru a misonkho kuti awasautse ndi akatunduno. Ndipo anammangira Farao midzi yosungiramo cuma, ndiyo Pitomu ndi Ramese.