Exodus 1:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Aisraele ankati akamaŵazunza kwambiri, ndi pamene iwo tsono ankachulukirachulukira, mpaka adabalalikira m'dziko lonselo. Motero Aejipito ankaŵaopa Aisraele,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma monga momwe anawasautsiramo, momwemo anachuluka, momwemonso anafalikira. Ndipo anavutika chifukwa cha ana Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma pamene ankawazunza kwambiri, Aisraeli ndiye ankachulukirachulukira mpaka kubalalikira mʼdziko lonse. Kotero Aigupto anayamba kuopa Aisraeliwo
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma monga momwe anawasautsiramo, momwemo anacuruka, momwemonso anafalikira. Ndipo anabvutika cifukwa ca ana a Israyeli.