Exodus 1:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Moyo wa Aisraele unali woŵaŵa chifukwa cha ntchito yakalavulagaga youmba njerwa, ndiponso ntchito zosiyanasiyana zam'minda. Ankaŵakakamiza mwankhanza kugwira ntchito zonse zolemetsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nawawitsa moyo wao ndi ntchito yolimba, ya dothi ndi ya njerwa, ndi ntchito zonse za pabwalo, ntchito zao zonse zimene anawagwiritsa nzosautsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aigupto anachititsa moyo wa Aisraeli kukhala owawa kwambiri powagwiritsa ntchito yakalavulagaga yowumba njerwa ndi kuponda dothi lomangira, pamodzi ndi ntchito zina zosiyanasiyana zamʼminda. Iwo anakakamiza Aisraeli mwankhanza kuti agwire ntchito yowawayi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nawawitsa moyo wao ndi nchito yolimba, ya dothi ndi ya njerwa, ndi nchito zonse za pabwalo, nchito zao zonse zimene anawagwiritsa nzosautsa.