Exodus 1:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Azamba aja adayankha kuti “Azimai achihebri safanafana ndi azimai achiejipito. Iwo ngamphamvu, amati mzamba asanafike, mwana amakhala atabadwa kale.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamwino ananena ndi Farao, Popeza akazi a Ahebri safanana ndi akazi a Aejipito; pakuti ali ndi mphamvu, naona ana asanafike anamwino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Azambawo anamuyankha Farao kuti, “Amayi a Chihebri sali ngati amayi a Chiigupto; Iwo ndi amphamvu ndipo amachira azamba asanafike.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamwino ananena ndi Farao, Popeza akazi a Ahebri safanana ndi akazi a Aigupto; pakuti ali ndi mphamvu, naona ana asanalike anamwino.