Exodus 1:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma adzukulu a Aisraele adabala ana ambirimbiri. Adachulukana nakhala amphamvu kwambiri nkudzaza dzikolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ana a Israele ndipo anaswana, nabalana, nachuluka, nakhala nazo mphamvu zazikulu; ndipo dziko linadzala nao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Aisraeli anaberekana ndi kuchuluka kwambiri nakhala amphamvu kwambiri, kotero kuti anadzaza dzikolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ana a Israyeli ndipo anaswana, nabalana, nacuruka, nakhala nazo mphamvu zazikuru; ndipo dziko linadzala nao.