Exodus 10:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ai! Inu, amuna nokhanu, ndiye mupite mukapembedze Chauta, popeza kuti ndi zimene mukufuna.” Atangomveka mau ameneŵa, Mose ndi Aroni adapirikitsidwa pamaso pa Farao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chotero ai, mukani tsopano, inu amuna akulu, tumikirani Yehova pakuti ichi muchifuna. Ndipo anawapirikitsa pamaso pa Farao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndakana! Amuna okha ndiwo apite ndi kukapembedza Yehova pakuti izi ndi zimene mwakhala mukupempha.” Kenaka Mose ndi Aaroni anathamangitsidwa pamaso pa Farao.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cotero ai, mukani tsopano, inu amuna akuru, tumikirani Yehova pakuti ici mucifuna. Ndipo anawapitikitsa pamaso pa Farao.