Exodus 10:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Tambalitsa dzanja lako pa dziko la Ejipito kuti dzombe libwere, ndipo lidzadye zomera zonse zimene matalala aja adasiya.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasulira dzanja lako pa dziko la Ejipito, lidze dzombe, kuti likwere pa dziko la Ejipito, lidye zitsamba zonse za m'dziko, ndizo zonse adazisiya matalala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Tambalitsa dzanja lako pa dziko la Igupto kuti dzombe lidze pa dziko la Igupto ndi kuwononga chilichonse chimene chikumera mʼminda ndi chilichonse chimene chinatsala pa nthawi ya matalala.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasulira dzanja lako pa dziko la Aigupto, lidze dzombe, kuti likwere pa dziko la Aigupto, lidye zitsamba zonse za m'dziko, ndizo zonse adazisiya matalala.