Exodus 10:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Lidangophimba dziko lonse, ndipo lidakhazikika m'dzikomo. Kuchuluka kwake kwa dzombelo kunali kwakuti nkale lonse dzombe lotero silidaonekepo, ndipo silidzaonekanso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo dzombe linakwera pa dziko lonse la Ejipito, ndipo linatera pakati pa malire onse Ejipito, lambirimbiri; lisanafike ili panalibe dzombe lotere longa ili, ndipo litapita ili sipadzakhalanso lotere.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dzombelo linafika pa dziko lonse la Igupto ndi kukhala dera lililonse la dzikolo. Dzombe lambiri ngati limenelo silinakhaleponso nʼkale lonse ndipo silidzakhalapo ngakhale mʼtsogolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo dzombe linakwera pa dziko lonse la Aigupto, ndipo linatera pakati pa malire onse a Aigupto, lambirimbiri; lisanafike ili panalibe dzombe lotere longa ili, ndipo litapita ili sipadzakhalanso lotere.